2 Kings 4:23 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo mwamuna wakeyo adafunsa kuti, “Chifukwa chiyani mukupita kwa iyeyo lero? Lerotu si tsiku lokhala mwezi, kapenanso tsiku la Sabata ai.” Mai uja adati, “Palibe kanthu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anati, Ulikumuka kwa iye lero chifukwa ninji? Ngati mwezi wakhala, kapena mpa Sabata? Koma anati, Kuli bwino.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mwamuna wakeyo anafunsa kuti, “Chifukwa chiyani ukupita kwa iyeyo lero? Lero si tsiku la Chikondwerero cha Mwezi Watsopano kapena tsiku la Sabata.” Mayiyo anayankha kuti, “Zonse zili bwino.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anati, Ulikumuka kwa iye lero cifukwa ninji? ngati mwezi wakhala, kapena: mpa sabata? Koma anati, Kuli bwino.