2 Kings 4:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero adayenda nakafika kwa Elisa, munthu wa Mulungu uja, ku phiri la Karimele. Tsono mneneri Elisa ataona kuti mai uja akudza, adauza Gehazi mtumiki wake kuti, “Taona patsidyapo, Msunamu uja akubwera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Potero anamuka, nafika kwa munthu wa Mulungu kuphiri la Karimele. Ndipo kunali, pakumuona munthu wa Mulungu alinkudza kutali, anati kwa Gehazi mnyamata wake, Tapenya, suyo Msunamu uja;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho ananyamuka nakafika kwa munthu wa Mulungu uja ku Phiri la Karimeli. Munthu wa Mulungu ataona mayiyo patali, anawuza mtumiki wake Gehazi kuti, “Taona! Msunemu uyo!
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Potero anamuka, nafika kwa munthu wa Mulungu ku phiri la Karimeli. Ndipo kunali, pakumuona munthu wa Mulungu alinkudza kutali, anati kwa Gehazi mnyamata wace, Tapenya, suyo Msunemu uja;