2 Kings 4:27 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono atafika kuphiriko kwa Elisa munthu wa Mulungu uja, maiyo adagwada, nagwira mapazi a Elisa. Gehazi adadza kuti amkankhe. Koma Elisa adati, “Mleke, kodi sukuwona kuti ali pa mavuto aakulu? Chauta wandibisira ine zimenezi, sadandiwuze.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pofika kwa munthu wa Mulungu kuphiri anamgwira mapazi. Ndipo Gehazi anayandikira kuti amkankhe; koma munthu wa Mulungu anati, Umleke, pakuti mtima wake ulikumuwawa; ndipo Yehova wandibisira osandiuza ichi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atafika kwa munthu wa Mulunguyo pa phiripo, mayiyo anagwira mapazi a Elisa. Gehazi anabwera kuti amukankhe, koma munthu wa Mulungu anati, “Musiye! Iyeyu ali pa mavuto aakulu, koma Yehova wandibisira zimenezi ndipo sanandiwuze chifukwa chake.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pofika kwa munthu wa Mulungu kuphiri anamgwira mapazi. Ndipo Gehazi anayandikira kuti amkankhe; koma munthu wa Mulungu anati, Umleke, pakuti mtima wace ulikumwawa; ndipo Yehova wandibisira osandiuza ici.