2 Kings 4:29 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Elisa adauza Gehazi kuti, “Vala lamba wako, fulumira, utenge ndodo yanga ndipo upite. Ukakumana ndi munthu wina aliyense pa njira, usampatse moni, ndipo wina aliyense akakupatsa moni, usayankhe. Tsono ukagoneke ndodo yangayi pa nkhope ya mwanayo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo anati kwa Gehazi, Udzimangire m'chuuno, nutenge ndodo yanga m'dzanja lako, numuke; ukakomana ndi munthu usampatse moni; wina akakupatsa moni usamyankhe; ukaike ndodo yanga pankhope pa mwanayo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Elisa anawuza Gehazi kuti, “Manga lamba mʼchiwuno mwako, tenga ndodo yanga mʼdzanja lako ndipo thamanga. Ngati ukumana ndi munthu wina aliyense, usamupatse moni, ndipo ngati wina akupatsa moni, usayankhe. Ukagoneke ndodo yanga pa nkhope ya mwanayo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo anati kwa Gehazi, Udzimangire m'cuuno, nutenge ndodo yanga m'dzanja lako, numuke; ukakomana ndi munthu usamlankhule; akakulankhula wina usamyankhe; ukaike ndodo yanga pankhope pa mwanayo.