2 Kings 4:31 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Gehazi adatsogolako, ndipo adakaigoneka ndodoyo pa nkhope ya mwana uja, koma sipadamveke mau kapena kuwoneka chizindikiro china cha moyo. Choncho Gehaziyo adangobwerera kukakumana ndi Elisa, ndipo adamuuza kuti, “Mwana uja sadauke ai.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nawatsogolera Gehazi, naika ndodo pankhope pa mwanayo; koma mwanayo analibe mau, kapena kusamalira. Motero anabwerera kukomana naye, namuuza kuti, Sanauke mwanayo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Gehazi anatsogola nakagoneka ndodoyo pa nkhope ya mwanayo, koma sipanamveke mawu kapena kugwedezeka kuonetsa kuti ali moyo. Choncho Gehazi anabwerera kukakumana ndi Elisa ndipo anamuwuza kuti, “Mwanayo sanatsitsimuke.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nawatsogolera Gehazi, naika ndodo pankhope pa mwanayo; koma mwanayo analibe mau, kapena kusamalira. Motero anabwerera kukomana naye, namuuza kuti, Sanauke mwanayo.