2 Kings 4:34 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono adakamgonera mwanayo, nakhudzitsa pakamwa pake ndi pakamwa pa mwanayo. Ndipo m'mene ankadzitambalitsa choncho pa mwanayo, thupi la mwana uja lidayamba kufunda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nakwera, nagona pa mwanayo ndi kulinganiza pakamwa pake ndi pakamwa pake, maso ake ndi maso ake, zikhato zake ndi zikhato zake, nadzitambasula pa iye, ndi mnofu wa mwana unafunda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka anakwera pa bedi ndi kumugonera mwanayo, pakamwa pake panakhudzana ndi pakamwa pa mwanayo, maso ake anakhudzana ndi maso a mwanayo, ndipo manja ake anakhudzana ndi manja a mwanayo. Pamene ankadzitambalitsa yekha pa mwanayo, thupi la mwanayo linayamba kufunda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nakwera, nagona pa mwanayo ndi kulinganiza pakamwa pace ndi pakamwa pace, maso ace ndi maso ace, zikhato zace ndi zikhato zace, nadzitambasula pa iye, ndi mnofu wa mwana unafunda.