2 Kings 4:40 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono adapakula naŵapatsa anthuwo kuti adye. Koma pamene adayamba kudya chakudyacho, anthuwo adafuula kuti, “Inu, munthu wa Mulungu, muli dziphe m'nkhalimu.” Choncho sadathe kudya chakudyacho.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo anagawira anthu kuti adye. Koma kunali, pakudya chakudyacho, anafuula nati, Munthu wa Mulungu, muli imfa m'nkhalimo. Ndipo sanathe kudyako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anawapakulira anthu chakudyacho, koma atayamba kudya, anthuwo anafuwula kuti, “Inu munthu wa Mulungu muli imfa mu mʼphikamu!” Ndipo sakanatha kudya chakudyacho.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo anagawira anthu kuti adye. Koma kunali; pakudya cakudyaco, anapfuula nati, Munthu wa Mulungu, muli imfa m'nkhalimo. Ndipo sanatha kudyako.