2 Kings 4:41 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Elisa adaŵauza kuti, “Bwerani ndi ufa.” Elisayo adathira ufawo m'nkhali nati, “Apakulireninso anthu chakudyacho kuti adye.” Ndipo adapeza kuti munalibenso zoopsa m'nkhali muja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo anati, Bwera naoni ufa. Nathira m'nkhalimo; nati, Gawirani anthu kuti adye. Ndipo m'nkhalimo munalibe chowawa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Elisa anati, “Bweretsani ufa.” Iye anathira ufa mu mʼphikamo ndipo anati, “Perekani chakudyachi kwa anthu kuti adye.” Ndipo mu mʼphikamo munalibenso zoopsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo anati, Bwera naoni ufa. Nathira m'nkhalimo; nati, Gawirani anthu kuti adye. Ndipo m'nkhalimo munalibe cowawa.