2 Kings 4:42 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku lina munthu wina wochokera ku Baala-Salira adabwera kwa Elisa atamtengerako buledi wopangidwa ndi zokolola zatsopano, mitanda makumi aŵiri ya buledi wa barele ndiponso ngala zatirigu zatsopano. Zonsezi adaazitengera m'thumba mwake. Tsono Elisa adati, “Agaŵire anthu chakudyachi kuti adye.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anadza munthu kuchokera ku Baala-Salisa, nabwera nayo m'thumba mikate ya zipatso zoyamba kwa munthu wa Mulungu, mikate ya barele makumi awiri, ndi ngala zaziwisi za tirigu zosaomba. Ndipo anati, Uwapatse anthu kuti adye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Munthu wina wochokera ku Baala-Salisa anabwera atamutengera munthu wa Mulungu malofu a barele makumi awiri opangidwa kuchokera ku zokolola zoyamba kucha, pamodzinso ndi ngala zatsopano za tirigu. Elisa anati kwa munthuyo, “Apatse anthu kuti adye.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anadza munthu kucokera ku Baala Salisa, nabwera nayo mikate ya zipatso zoyamba kwa munthu wa Mulungu, mikate ya barele makumi awiri, ndi ngala zaziwisi za tirigu zosaomba. Ndipo anati, Uwapatse anthu kuti adye.