2 Kings 4:43 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma wantchito wake adamufunsa kuti, “Kodi chakudya chimenechi ndingachigaŵe motani kwa anthu 100 onseŵa?” Elisayo adanenanso kuti, “Apatseni anthuwo, pakuti Chauta akunena kuti, ‘Anthuwo adzadya ndipo chakudyacho chidzatsalako.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma mnyamata wake anati, Chiyani? Ndigawire amuna zana ichi kodi? Koma anati, Uwapatse anthu kuti adye; pakuti atero Yehova, Adzadya nadzasiyako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mtumiki wake anafunsa kuti, “Kodi ndikachigawe motani chakudyachi kwa anthu 100?” Koma Elisa anamuwuzanso kuti, “Apatse anthu adye. Pakuti izi ndi zimene Yehova akunena kuti, ‘Iwo adzadya chakudyachi ndipo china chidzatsalako.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma mnyamata wace anati, Ciani? ndigawire amuna zana ici kodi? Koma anati, Uwapatse anthu kuti adye; pakuti atero Yehova, Adzadya nadzasivako.