2 Kings 4:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mbiyazo zitadzaza zonse, maiyo adauza mwana wake kuti, “Bwera ndi inanso mbiya.” Koma mwanayo adauza mai wake kuti, “Palibenso ina.” Pomwepo mafuta aja adaleka kutuluka m'kambiya kaja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali, zitadzala zotengera, anati kwa mwana wake, Nditengere chotengera china. Nanena naye, Palibe chotengera china. Ndipo mafuta analeka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mitsuko yonse itadzaza, mayiyo anawuza mwana wake kuti, “Bweretsa mtsuko wina.” Koma iye anayankha kuti, “Mitsuko yonse yatha.” Pamenepo mafuta analeka kutuluka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali, zitadzala zotengera, anati kwa mwana wace, Nditengere cotengera cina, Nanena naye, Palibe cotengera cina. Ndipo mafuta analeka.