2 Kings 4:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku lina Elisa adapita ku Sunemu kumene kunkakhala mai wina wachuma. Maiyo adaumiriza Elisayo kuti adye chakudya kunyumba kwake. Motero Elisa ankati akamadzera njira imeneyo, nthaŵi zonse ankapatuka kunyumbako nkukadya nao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo linafika tsiku lakuti Elisa anapitirira kunka ku Sunemu, kumeneko kunali mkazi womveka; ameneyo anamuumiriza adye mkate. Potero pomapitirako iyeyo, ankawapatukirako kukadya mkate.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsiku lina Elisa anapita ku Sunemu. Kumeneko kunkakhala mayi wina wachuma amene anawumiriza Elisa kuti adye chakudya. Choncho nthawi iliyonse imene Elisa amadutsa kumeneko, ankayima ndi kudya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo linafika tsiku lakuti Elisa anapitirira kumka ku Sunemu, kumeneko kunali mkazi womveka; ameneyo anamuumiriza adye mkate. Potero pomapitirako iyeyu, adafowapa, mbukirako kukadya mkate.