2 Kings 5:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Panali mkulu wina wa gulu lankhondo la mfumu ya ku Siriya, dzina lake Naamani, amene anali munthu wokhulupirika kwambiri kwa mbuye wake. Mbuye wakeyo ankamkonda Naamaniyo kwambiri, chifukwa choti ankhondo ake ankapambana pa nkhondo, popeza kuti Chauta anali naye Naamaniyo. Naamaniyo anali munthu wamphamvu ndiponso wolimba mtima, koma anali wakhate.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Naamani kazembe wa khamu la nkhondo la mfumu ya Aramu anali munthu womveka pamaso pa mbuyake, ndi waulemu; popeza mwa iye Yehova adapulumutsa Aaramu; ndiyenso ngwazi, koma wakhate.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Naamani anali mtsogoleri wa gulu lankhondo a mfumu ya ku Aramu. Iye anali munthu wodalirika pamaso pa mbuye wake ndipo anali wokondedwa kwambiri, chifukwa kudzera mwa iye Yehova anapambanitsa Aaramu. Anali msilikali wolimba mtima, koma anali ndi khate.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Namani kazembe wa khamu la nkhondo la mfumu ya Aramu anali munthu womveka pamaso pa mbuyace, ndi waulemu; popeza mwa iye Yehova adapulumutsa Aaramu; ndiyenso ngwazi, koma wakhate.