2 Kings 5:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Naamani atamva zimenezi, adakwiya kwambiri nachokapo. Popita iye ankati, “Ha! Ine ndimaganiza kuti atuluka kubwera pano, ndipo aimirira natama dzina la Chauta Mulungu wake mopemba, naweyula dzanja lake pamwamba pa nthendapo, ndi kundichiritsa motero.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Naamani adapsa mtima, nachoka, nati, Taona, ndinati m'mtima mwanga, kutuluka adzanditulukira, nadzaima ndi kuitana pa dzina la Yehova Mulungu wake, ndi kuweyula dzanja lake pamalopo, ndi kuchiritsa wakhateyo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Naamani anachoka mokwiya ndipo anati, “Ine ndimaganiza kuti munthuyu atuluka ndipo ayimirira nayitana dzina la Yehova Mulungu wake, nayendetsa dzanja lake pamwamba pa nthendayi ndi kundichiritsa khate langa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Namani adapsa mtima, nacoka, nati, Taona, ndinati m'mtima mwanga, kuturuka adzanditurukira, nadzaima ndi kuitana pa dzina la Yehova Mulungu wace, ndi kuweyula dzanja lace pamalopo, ndi kuciritsa wakhateyo.