2 Kings 5:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma atumiki ake adasendera pafupi namufunsa kuti, “Pepani bambo, kodi mneneri akadakulamulani chinthu chachikulu, inu simukadachita? Monga nchapatali kukasamba monga momwe mneneriyo wakuuziranimo?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo anyamata ake anasendera, nanena naye, nati, Atate wanga, mneneri akadakuuzani chinthu chachikulu, simukadachichita kodi? Koposa kotani nanga ponena iye, Samba, nukonzeke?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Antchito ake anamuyandikira namufunsa kuti, “Abambo anga, mneneri akanakulamulani chinthu chachikulu, kodi inu simukanachita? Nanga nʼzovuta motani zomwe mneneri wanena kuti ‘Kasambeni ndipo mudzayeretsedwa!’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo anyamata ace anasendera, nanena naye, nati, Atate wanga, mneneri akadakuuzani cinthu cacikuru, simukadacicita kodi? koposa kotani nanga ponena iye, Samba, nukonzeke?