2 Kings 5:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero Naamaniyo adapita ku Yordani, nakakhuvula m'madzimo kasanunkaŵiri, malinga ndi m'mene adaamuuzira munthu wa Mulungu uja. Pompo adachira ndipo thupi lake lidangoti see ngati la kamwana, choncho adakhala woyeretsedwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Potero anatsika, namira m'Yordani kasanu ndi kawiri, monga adanena munthu wa Mulunguyo; ndi mnofu wake unabwera monga mnofu wa mwana wamng'ono, nakonzeka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Naamani anapita ku Yorodani nakadzimiza mʼmadzimo kasanu nʼkawiri, monga momwe munthu wa Mulungu anamuwuzira. Thupi lake linakhalanso monga kale ndipo linakhala losalala ngati la kamnyamata.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Potero anatsika, namira m'Yordano kasanu ndi kawiri, monga adanena munthu wa Mulunguyo; ndi mnofu wace unabwera monga mnofu wa mwana wamng'ono, nakonzeka.