2 Kings 5:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake Naamani pamodzi ndi onse omperekeza, adabwerera kwa mneneri wa Mulungu uja. Adadzaima pamaso pa Elisa namuuza kuti, “Ndithu, ine ndadziŵa tsopano kuti pa dziko lonse lapansi kulibe Mulungu wina, koma wa ku Israele yekha. Tsono landirani mphatsoyi kwa ine mtumiki wanu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo anabwerera kwa munthu wa Mulungu iye ndi gulu lake lonse, nadzaima pamaso pake, nati, Taonani, tsopano ndidziwa kuti palibe Mulungu pa dziko lonse lapansi, koma kwa Israele ndiko; ndipo tsopano, mulandire chakukuyamikani nacho kwa mnyamata wanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo Naamani ndi atumiki ake onse anabwerera kwa munthu wa Mulungu uja. Naamani anayima pamaso pa Elisa ndipo anati, “Tsopano ndikudziwa kuti kulibe Mulungu wina pa dziko lonse lapansi koma mu Israeli mokha. Chonde, tsopano landirani mphatso ya mtumiki wanu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamer nepo anabwerera kwa munthu wa Mulungu iye ndi gulu lace lonse, nadzaima pamaso pace, nati, Taonani, tsopano ndidziwa kuti palibe Mulungu pa dziko lonse lapansi, koma kwa Israyeli ndiko; ndipo tsopano, mulandire cakukuyamikani naco kwa mnyamata wanu.