2 Kings 5:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta andikhululukire ine pa chokhachi chakuti pamene mbuyanga mfumu akupita kukapembedza ku nyumba ya Chauta wake Rimoni, ine ndimatsagana naye ndipo ndimakagwada m'nyumba ya Rimoniyo. Chauta andikhululukire ine mtumiki wanu zimenezi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yehova akhululukire mnyamata wanu mwa ichi; akalowa mbuye wanga m'nyumba ya Rimoni kulambiramo, nakatsamira pa dzanja langa, nanenso ndikagwadira m'nyumba ya Rimoni, pakugwadira ine m'nyumba ya Rimoni, Yehova akhululukire mnyamata wanu mwa ichi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Yehova andikhululukire ine pa chinthu ichi: Pamene mbuye wanga alowa mʼnyumba ya mapemphero ya Rimoni ine ndimapita naye ndipo ndimakagwada naye limodzi. Pamene ndikugwada mʼnyumba ya mapemphero ya Rimoni, Yehova azikhululukira mtumiki wanu pa chinthu chimenechi.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yehova akhululukire mnyamata wanu mwa ici; akalowa mbuye wanga m'nyumba ya Rimoni kulambiramo, nakatsamira pa dzanja langa, nanenso ndikagwadira m'nyumba ya Rimoni, pakugwadira ine m'nyumba ya Rimoni, Yehova akhululukire mnyamata wanu mwa ici.