2 Kings 5:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Naamani atangoyenda mtunda pang'ono, Gehazi, mtumiki wa Elisa mneneri wa Mulungu, adayamba kulingalira kuti, “Mbuyanga walekerera Naamani Msiriyayu, osalandira zimene adabwera nazo kudzapereka. Pali Chauta, Mulungu wamoyo, ine ndimthamangira kuti ndikalandireko kanthu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Gehazi, mnyamata wa Elisa, munthu wa Mulungu, anati, Taona, mbuye wanga analekera Naamani uyu wa ku Aramu osalandira m'manja ake chimene anabwera nacho; pali Yehova, ndidzathamangira ndi kulandira kanthu kwa iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Gehazi, mtumiki wa Elisa munthu wa Mulungu, anaganiza mu mtima mwake kuti, “Taonani, mbuye wanga wamulekerera Naamani Mwaramuyu, posalandira zomwe anabweretsa. Pali Yehova wamoyo, ine ndimuthamangira ndipo ndikatengako zinthu kwa iye.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Gehazi, mnyamata wa Elisa, munthu wa Mulungu, anati, Taona, mbuye wanga analekera Namani uyu wa ku Aramu osalandira m'manja ace cimene anabwera naco; pali Yehova, ndidzathamangira ndi kulandira kanthu kwa iye.