2 Kings 5:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero Gehazi adalondola Naamani uja. Naamani ataona kuti munthu akumthamangira, adatsika pa galeta kuti amchingamire. Tsono adafunsa kuti “Kodi nkwabwino?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Motero Gehazi anatsata Naamani. Ndipo pamene Naamani anaona wina alikumthamangira, anatsika pagaleta kukomana naye, nati, Nkwabwino kodi?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Gehazi anamuthamangira Naamani uja. Naamani ataona Gehazi akumuthamangira, anatsika mʼgaleta lake ndi kukakumana naye. Iye anafunsa Gehazi kuti, “Kodi nʼkwabwino?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Motero Gehazi anatsata Namani. Ndipo pamene Namani anaona wina alikumthamangira, anatsika pagareta kukomana naye, nati, Nkwabwino kodi?