2 Kings 5:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Gehazi adati, “Inde, nkwabwino. Koma mbuyanga wandituma chifukwa tsopano apa kwangomufikira anthu aŵiri a m'gulu la aneneri, kuchokera ku dziko lamapiri la Efuremu. Tsono akukupemphani kuti chonde muŵapatseko ndalama zasiliva 3,000 ndi zovala ziŵiri zapaphwando.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nati, Kuli bwino. Mbuye wanga wandituma, ndi kuti, Taonani, andifikira tsopano apa anyamata awiri a ana a aneneri, ochokera ku mapiri a Efuremu; muwapatse talente wa siliva, ndi zovala zosintha ziwiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Gehazi anayankha kuti, “Inde nʼkwabwino. Mbuye wanga wandituma kuti ndidzakuwuzeni kuti, ‘Anyamata awiri mwa ana a aneneri angondipeza kumene kuchokera ku dziko la mapiri la Efereimu. Chonde apatseniko ndalama za siliva 3,000 ndi zovala ziwiri za pa phwando.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nati, Kuli bwino. Mbuye wanga wandituma, ndi kuti, Taonani, andifikira tsopano apa anyamata awiri a ana a aneneri, ocokera ku mapiri a Efraimu; muwapatse talente wa siliva, ndi zobvala zosintha ziwiri.