2 Kings 5:24 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Gehazi uja atafika kuphiri kumene kunali nyumba ya Elisa, adaŵalanda antchitowo ndalama zija nazilonga m'nyumba mwake. Ndipo adaŵauza kuti apite, iwo nkupita.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene anafika kumsanje anazilandira m'manja mwao, naziika m'nyumba; nauza anthuwo amuke, iwo nachoka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Gehazi atafika ku phiri, anawalanda antchito aja zinthu zija nazibisa mʼnyumbamo. Iye anawawuza anthu aja kuti abwerere ndipo anapita.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene anafika kumsanje anazilandira m'manjamwao, naziika m'nyumba; nauza anthuwo amuke, iwo nacoka.