2 Kings 5:26 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Elisayo adamufunsanso kuti, “Kodi ukuyesa kuti sindidakuwone monse muja munthu uja amatsika pa galeta kuti adzakuchingamire? Kodi imeneyi inali nthaŵi yolandira ndalama ndi zovala, minda ya olivi ndi ya mphesa, kapena ng'ombe, akapolo kapena adzakazi?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anati kwa iye, Mtima wanga sunakuperekeza kodi, umo munthuyo anatembenuka pa galeta wake kukomana ndi iwe? Kodi nyengo yino ndiyo yakulandira siliva, ndi kulandira zovala, ndi minda ya azitona, ndi yampesa, ndi nkhosa, ndi ng'ombe, ndi akapolo, ndi adzakazi?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Elisa anati kwa Gehazi, “Kodi mzimu wanga sunali nawe pamene munthu uja anatsika mʼgaleta lake ndi kukumana nawe? Kodi ino ndi nthawi yolandira ndalama, kapena kulandira zovala, mitengo ya olivi, minda ya mpesa, nkhosa, ngʼombe kapena antchito aamuna kapena antchito aakazi?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anati kwa iye, Mtima wanga sunakuperekeza kodi, umo munthuyo anatembenuka pa gareta wace kukomana ndi iwe? Kodi nyengo yino ndiyo yakulandira siliva, ndi kulandira zobvala, ndi minda yaazitona, ndi yampesa, ndi nkhosa, ndi ng'ombe, ndi akapolo; ndi adzakazi?