2 Kings 5:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atafika kwa mfumu ya ku Israele, adapereka kalata ija imene mau ake anali akuti, “Landirani kalatayi. Tsono amene ndakutumiziraniyo ndi Naamani mtumiki wanga, ndipo ndikufuna kuti inuyo mumchize khate lake.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anafika kwa mfumu ya Israele ndi kalata, wakuti, Pakulandira kalata uyu, taonani, ndatumiza Naamani mnyamata wanga kwa inu, kuti mumchiritse khate lake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kalata imene anapita nayo kwa mfumu ya ku Israeli inali ndi mawu awa: “Taonani, ndikutumiza Naamani mtumiki wanga pamodzi ndi kalatayi kwa inu kuti mumuchiritse khate lake.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anafika kwa mfumu ya Israyeli ndi kalata, wakuti, Pakulandira kalata uyu, taonani, ndatumiza Namani mnyamata wanga kwa inu, kuti mumciritse khate lace.