2 Kings 5:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma mfumu ya ku Israele ija itaŵerenga kalatayo, idang'amba zovala zake chifukwa cha chisoni, ndipo idati, “Kodi ine ndine Mulungu amene amapha ndi kupatsanso moyo, kuti munthu ameneyu azindilembera mau oti ndichize khate la munthu wake? Nchodziŵikiratu kuti iyeyo akungofuna chifukwa choti ayambane nane.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali atawerenga kalatayu mfumu ya Israele, anang'amba zovala zake, nati, Ngati ndine Mulungu, kupha ndi kubwezera moyo, kuti ameneyo atumiza kwa ine kumchiritsa munthu khate lake? Pakuti dziwani, nimupenye, kuti alikufuna chifukwa pa ine.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu ya ku Israeli itangowerenga kalatayo, inangʼamba mkanjo wake ndipo inati, “Kodi ine ndine Mulungu? Kodi ndingathe kupha kapena kupereka moyo? Chifukwa chiyani munthu ameneyu wanditumizira munthu woti ndimuchiritse khate lake? Taonani, iyeyu akungofuna kuti apeze chifukwa choyambanirana nane!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali atawerenga kalatayu mfumu ya Israyeli, anang'amba zobvala zace, nati, Ngati ndine Mulungu, kupha ndi kubwezera moyo, kuti ameneyo atumiza kwa ine kumciritsa munthu khate lace? pakuti dziwani, nimupenye, kuti alikufuna cifukwa pa ine.