2 Kings 5:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma mneneri Elisa atamva kuti mfumu ya ku Israele idang'amba zovala zake, adatumiza mau kwa mfumuyo akuti, “Chifukwa chiyani mwang'amba zovala zanu? Alendowo abwere kwa ine tsopano lino, kuti adziŵe kuti ku Israele kuli mneneri.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma kunali, pamene Elisa munthu wa Mulungu anamva kuti mfumu ya Israele adang'amba zovala zake, anatumiza mau kwa mfumu, ndi kuti, Mwang'amba zovala zanu chifukwa ninji? Adzetu kwa ine, ndipo adzadziwa kuti muli mneneri m'Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Elisa munthu wa Mulungu atamva kuti mfumu ya ku Israeli yangʼamba mkanjo wake, anatumiza uthenga uwu: “Chifukwa chiyani mwangʼamba mkanjo wanu? Mutumizeni munthuyo kwa ine ndipo iyeyo adzadziwa kuti muli mneneri mu Israeli.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma kunali, pamene Elisa munthu wa Mulungu anamva kuti mfumu ya Israyeli adang'amba zobvala zace, anatumiza mau kwa mfumu, ndi kuti, Mwang'amba zobvala zanu cifukwa ninji? Adzetu kwa ine, ndipo adzadziwa kuti muli mneneri m'Israyeli.