2 Kings 6:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono mfumu ya ku Israele idatuma anthu ku malo amene mneneri wa Mulungu uja adaanenaŵa. Umu ndimo m'mene mneneri ankachenjezera mfumu, kotero kuti idapulumuka kangapo konse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo mfumu ya Israele inatumiza kumene munthu wa Mulungu anamuuzako ndi kumchenjeza; nadzisunga osapitako, kawirikawiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho mfumu ya ku Israeli inatuma anthu kumalo kumene munthu wa Mulunguyo ananena. Nthawi ndi nthawi Elisa ankachenjeza mfumu, kotero kuti ankakhala tcheru ku malo amenewo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo mfumu ya Israyeli inatumiza kumene munthu wa Mulungu anamuuzako ndi kumcenjeza; nadzisunga osapitako, kawiri kawiri.