2 Kings 6:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono mfumu ya ku Siriya inkavutika kwambiri mu mtima chifukwa cha zimenezi. Choncho idaitana aphungu ake niŵafunsa kuti, “Kodi simungandiwuze pakati pathu pano munthu amene akuthandizira mfumu ya ku Israele?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma mtima wa mfumu ya Aramu unavutika kwambiri pa ichicho, naitana anyamata ake, nanena nao, Kodi simudzandiuza wina wa ife wovomerezana ndi mfumu ya Israele ndani?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zimenezi zinakwiyitsa kwambiri mfumu ya ku Aramu. Mfumuyo inayitanitsa atsogoleri ake ankhondo ndipo inawafunsa kuti, “Kodi simungandiwuze munthu amene pakati pathu pano ali mbali ya mfumu ya ku Israeli?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma mtima wa mfumu ya Aramu unabvutika kwambiri pa icico, naitana anyamata ace, nanena nao, Kodi simudzandiuza wina wa ife wobvomerezana ndi mfumu ya Israyeli ndani?