2 Kings 6:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mmodzi mwa aphunguwo adayankha kuti, “Palibe ndi mmodzi yemwe, inu mbuyanga mfumu. Koma Elisa mneneri wa ku Israele ndiye amene amauza mfumu ya ku Israele mau amene inuyo mumalankhula kumbali m'chipinda mwanu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nati mmodzi wa anyamata ake, Iai, mbuye wanga mfumu; koma Elisa, mneneriyo ali ku Israele ndiye amafotokozera mfumu ya Israele mau muwanena m'kati mwake mwa chipinda chanu chogonamo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mmodzi mwa atsogoleri a ankhondowo anati, “Palibe ndi mmodzi yemwe pakati pathu, inu mbuye wanga, koma Elisa mneneri amene ali ku Israeli amawuza mfumu ya ku Israeli mawu enieni amene inu mumayankhula ku chipinda kwanu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nati mmodzi wa anyamata ace, lai, mbuye wanga mfumu; koma Elisa, mneneriyo ali ku Israyeli, ndiye amafotokozera mfumu ya Israyeli mau muwanena m'kati mwace mwa cipinda canu cogonamo.