2 Kings 6:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono wantchito wa munthu wa Mulungu uja, atadzuka m'mamaŵa nkutuluka, adangoona gulu lankhondo lokwera pa akavalo ndi magaleta, litazinga mzinda wonsewo. Pomwepo wantchitoyo adabwerera nati, “Kalanga ine mbuyanga! Kodi titani?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo atalawirira mamawa mnyamata wa munthu wa Mulungu, natuluka, taonani, khamu la nkhondo linazinga mudzi ndi akavalo ndi magaleta. Ndi mnyamata wake ananena naye, Kalanga ine, mbuye wanga! Tichitenji?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mtumiki wa munthu wa Mulungu atadzuka mmamawa ndi kutuluka panja, gulu la ankhondo pamodzi ndi akavalo ndi magaleta anali atazungulira mzindawo. Mtumikiyo anafunsa kuti, “Kalanga mbuye wanga, tidzachita chiyani?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo atalawirira mamawa mnyamata wa munthu wa Mulungu, naturuka, taonani, khamu la nkhondo linazinga mudzi ndi akavalo ndi magareta. Ndi mnyamata wace ananena naye, Kalanga ine, mbuye wanga! ticitenji?