2 Kings 6:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono pamene Asiriya adayamba kumthira nkhondo Elisa, iye adapemphera kwa Chauta, adati, “Ndikukupemphani kuti muŵachititse khungu anthu ameneŵa.” Motero Chauta adachititsa ankhondo aja khungu, monga momwe Elisa adapemphera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo atatsikira pali iye, Elisa anapemphera kwa Yehova, nati, Mukanthe mtundu uwu uchite khungu. Ndipo Iye anawakantha, nawachititsa khungu, monga mwa mau a Elisa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene adaniwo ankabwera kudzalimbana naye, Elisa anapemphera kwa Yehova kuti, “Achititseni khungu anthu awa.” Kotero Yehova anawachititsa khungu monga anapemphera Elisa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo atatsikira pali iye, Elisa anapemphera kwa Yehova, nati, Mukanthe mtundu uwu ucite khungu. Ndipo iye anawakantha, nawacititsa khungu, monga mwa mau a Elisa.