2 Kings 6:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atangoloŵa mu mzinda wa Samariyawo, Elisa uja adapemphera kuti, “Inu Chauta, atsekuleni maso anthuŵa apenye.” Choncho Chauta adatsekuladi maso ao, napenya. Ndipo adangoona kuti ali m'kati mwenimweni mwa Samariya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali, pakufika ku Samariya, Elisa anati, Yehova, muwakanganulire awa maso kuti aone. Nawakanganulira Yehova maso ao, naona iwo, ndipo tapenyani, ali pakati pa Samariya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atalowa mu mzinda wa Samariya, Elisa anati, “Yehova tsekulani maso a anthu awa kuti aone.” Choncho Yehova anatsekula maso awo ndipo anangoona kuti ali mʼkati mwenimweni mwa Samariya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali, pakufika ku Samariya, Elisa anati, Yehova, muwakanganulire awa maso kuti aone. Nawakanganulira Yehova maso ao, naona iwo, ndipo tapenyani, ali pakati pa Samariya.