2 Kings 6:23 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero adaŵakonzera madyerero aakulu. Atadya ndi kumwa, mfumuyo idaŵalola ankhondowo kuti achoke, ndipo iwo adapita kwa mbuyao. Pambuyo pake magulu ankhondo a Asiriya adaleka kuthira nkhondo dziko la Israele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anawakonzera chakudya chambiri, nadya namwa iwo; nawauza amuke; namuka kwa mbuye wao. Ndipo magulu a Aramu sanadzenso ku dziko la Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho anawakonzera mphwando lalikulu, ndipo atatsiriza kudya ndi kumwa, anawatumiza kwawo ndipo anabwerera kwa mbuye wawo. Kotero magulu a ankhondo a ku Aramu analeka kuthira nkhondo dziko la Israeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anwakonzera cakudya cambiri, nadya namwa iwo; nawauza amuke; namuka kwa mbuye wao. Ndipo magulu a Aramu sanadzanso ku dziko la Israyeli.