2 Kings 6:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ku Samariyako kunali njala yoopsa pa nthaŵi imene Asiriya ankazinga mzindawo ndi zithando zankhondo, mpaka kuti mutu wa bulu ankaugula ndi ndalama zasiliva 80. Ndipo magaramu 200 a zitosi za nkhunda ankagulitsa pamtengo wa masekeli asiliva asanu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma m'Samariya munali njala yaikulu; ndipo taonani, anaumangira misasa mpaka mutu wa bulu unagulidwa masekeli a siliva makumi asanu ndi atatu; ndi limodzi la magawo anai la muyeso wa kabu wa zitosi za nkhunda linagulidwa ndi masekeli asiliva asanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mu mzinda wa Samariya munali njala yoopsa. Ndipo taonani, Aaramu anazungulira mzindawu kwa nthawi yayitali kotero kuti mutu wa bulu ankawugulitsa ndalama za siliva 80, ndipo magalamu 200 a zitosi za nkhunda ankawagulitsa pa mtengo wa masekeli asanu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma m'Samariya munali njala yaikuru; ndipo taonani, anaumangira misasa mpaka mutu wa buru unagulidwa ndalama zasiliva makumi asanu ndi atatu; ndi limodzi la magawo anai la muyeso wa zitosi za nkhunda linagulidwa ndi ndalama zasiliva zisanu.