2 Kings 6:27 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo mfumuyo idafunsa kuti, “Kodi Chauta akapanda kukuthandiza, nanga ine ndingazipeze kuti zokuthandizira? Kodi kwatsalako kanthu ngati ku malo opunthira tirigu kapena ku malo opondera mphesa?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nati iye, Akapanda kukuthandiza Yehova, ndikaona kuti kokuthandiza ine? Kudwale kodi, kapena popondera mphesa?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu inayankha kuti, “Ngati Yehova sakuthandiza iwe, ine thandizo lako ndingalipeze kuti? Kuchokera ku malo opunthira tirigu kodi? Kuchokera kumalo opsinyira mphesa kodi?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nati iye, Akapanda kukuthandiza Yehova, ndikaona kuti kokuthandiza ine? kudwale kodi, kapena popondera mphesa