2 Kings 6:30 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mfumuyo itamva mau a maiwo idang'amba zovala zake. Pamenepo nkuti mfumuyo ikuyenda pa khoma. Ndipo anthu adangoona kuti mfumuyo yavala chiguduli m'kati mwa zovala zake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pakumva mfumu mau a mkaziyo, anang'amba zovala zake alinkupita nayenda palinga, anthu napenya; ndipo taonani, pali chiguduli m'kati pa thupi lake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu itamva mawu a mayiyo, inangʼamba mkanjo wake. Pamene inkayenda pa khoma, anthu anayangʼana, ndipo anaona zovala zamʼkati, pakuti anavala chiguduli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pakumva mfumu mau a mkaziyo, anang'amba zobvala zace alinkupita nayenda palinga, anthu napenya; ndipo taonani, pali ciguduli m'kati pa thupi lace.