2 Kings 6:32 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵiyo Elisa adaakhala pansi m'nyumba mwake, ndipo akuluakulu anali naye limodzi. Tsono mfumu ija idatuma mmodzi mwa atumiki ake kuti akatenge Elisa. Koma wamthengayo asanafike, Elisa adauza akuluakulu aja kuti, “Ha! Wopha anthu uja watuma munthu kuti adzandidule mutu. Akangofika wamthengayo, inu mutseke chitseko, ndipo muchigwiritse, asaloŵe. Kodi mgugu ukumveka pambuyo pakewo si wa mbuyake?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Elisa anakhala pansi m'nyumba mwake, ndi akulu anakhala pansi pamodzi naye; ndipo mfumu inatuma munthu amtsogolere, koma asanafike kwa Elisa mthengayo, anati kwa akulu, Mwapenya kodi m'mene mwana uyu wambanda watumiza munthu kuchotsa mutu wanga? Taonani, pakufika mthengayo mutseke pakhomo, mumkankhe ndi chitseko. Kodi mapazi a mbuye wake samveka dididi pambuyo pake?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Elisa nʼkuti atakhala mʼnyumba mwake, ndipo akuluakulu anali naye limodzi. Mfumu inatuma munthu wina kuti imutsogolere, koma asanafike, Elisa anawuza akuluakuluwo kuti, “Kodi simukuona momwe wopha munthu uja watumizira munthu wina kuti adzadule mutu wanga? Taonani mthengayo akafika, mutseke chitseko ndipo muchigwiritsitse kuti asalowe. Kodi ndikumvawo pambuyo pake si mgugu wa mbuye wake?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Elisa anakhala pansi m'nyumba mwace, ndi akulu anakhala pansi pamodzi naye; ndipo mfumu inatuma munthu amtsogolere, koma asanafike kwa Elisa mthengayo, anati kwa akulu, Mwapenya kodi m'mene mwana uyu wambanda watumiza munthu kucotsa mutu wanga? taonani, pakufika mthengayo mutseke pakhomo, mumkankhe ndi citseko. Kodi mapazi a mbuye wace samveka dididi pambuyo pace?