2 Kings 6:33 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Elisayo akulankhulabe ndi akuluakuluwo, mfumu ija idafika, ndipo idati, “Mavuto ameneŵa watigwetsera ndi Chauta. Kodi ndingathe bwanji kudikira thandizo lochokera kwa Chauta?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Akali chilankhulire nao, tapenyani, wamtsikira mthengayo; ndi mfumu inati, Taonani, choipa ichi chichokera kwa Yehova; ndilindiranjinso Yehova?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Elisa akuyankhulabe ndi anthuwo, taonani, wamthengayo anafika kwa iye. Ndipo mfumu inati, “Mavuto amenewa ndi ochokera kwa Yehova. Kodi nʼchifukwa chiyani ine ndiyenera kudikira thandizo lochokera kwa Yehova?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Akali cilankhulire nao, tapenyani, wamtsikira mthengayo; ndi mfumu inati, Taonani, coipa ici cicokera kwa Yehova; ndilindiranjinso Yehova?