2 Kings 6:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma pamene wina ankagwetsa nsichi, nkhwangwa yake idaguluka nigwa m'madzi, ndipo adafuula kuti, “Kalanga ine mbuyanga! Ndipotu nkhwangwa imeneyi njobwereka!”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo wina analinkudula mtengo nkhwangwa inagwa m'madzi; ndipo anafuula, nati, Kalanga ine mbuyanga! Popeza njobwereka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene wina ankadula mtengo, nkhwangwa yake inaguluka nigwera mʼmadzi. Iye anafuwula kuti, “Mayo! Mbuye wanga! Popeza ndi yobwereka!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo wina analinkudula mtengo nkhwangwa inagwa m'madzi; ndipo anapfuula, nati, Kalanga ine mbuyanga! popeza ojobwereka.