2 Kings 6:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma mneneri Elisa adatumiza mau kwa mfumu ya ku Israele kuti, “Chenjerani ku malo akutiakutiŵa, poti Asiriya akukabisala kumeneko.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo munthu wa Mulunguyo anatuma mau kwa mfumu ya Israele, ndi kuti, Muchenjere musapite pakuti, popeza Aaramu alikutsikira uko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Munthu wa Mulungu anatumiza mawu kwa mfumu ya ku Israeli kuti “Musamale podutsa malo akuti, chifukwa Aaramu akupita kumeneko.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo munthu wa Mulunguyo anatuma mau kwa mfumu ya Israyeli, ndi kuti, Mucenjere musapite pakuti, popeza Aaramu alikutsikira uko.