2 Kings 7:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Elisa adayankha nati, “Mverani, zimene akunena Chauta ndi izi, akuti, ‘Maŵa pa nthaŵi ngati yomwe ino makilogramu atatu a ufa wosalala adzaŵagulitsa pamtengo wa ndalama imodzi yasiliva, ndipo makilogramu asanu ndi limodzi a barele adzaŵagulitsanso pamtengo wa ndalama imodzi yasiliva ku chipata cha ku Samariya’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Elisa anati, Mverani mau a Yehova; atero Yehova, Mawa dzuwa lino adzagula muyeso wa ufa ndi sekeli, adzagulanso miyeso iwiri ya barele ndi sekeli, pa chipata cha Samariya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Elisa anati, “Mverani mawu a Yehova. Yehova akuti, ‘Mawa nthawi ngati yomwe ino, makilogalamu atatu a ufa adzawagulitsa pa mtengo wa ndalama imodzi yasiliva, ndipo makilogalamu asanu ndi limodzi a barele adzawagulitsa pa mtengo wa ndalama imodzi yasiliva ku chipata cha Samariya.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Elisa anati, Mverani mau; a Yehova; atero Yehova, Mawa dzuwa lino adzagula muyeso wa ufa ndi sekeli, adzagulanso miyeso iwiri ya barele ndi sekeli, pa cipata ca Samariya.