2 Kings 7:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero adapita ku Samariya nakaitana alonda a pa chipata cha mzinda naŵauza kuti, “Ife tidaapita ku zithando za Asiriya, ndipo tidangoona kuti kulibe munthu ndi mmodzi yemwe. Ngakhale kumva mau sitidamve, koma tidangopeza akavalo okha pamodzi ndi abulu ali chimangire, ndiponso mahema monga momwe adaaliri.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nadza iwo, naitana mlonda wa mudzi, namfotokozera; ndi kuti, Tinafika ku misasa ya Aaramu, ndipo taonani, palibe munthu pomwepo, kapena mau a munthu, koma akavalo omanga, ndi abulu omanga, ndi mahema ali chimangire.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho anapita nakayitana alonda a pa chipata cha mzinda ndi kufotokoza kuti, “Ife tinapita ku msasa wa Aaramu ndipo sitinapezeko munthu, kapena phokoso la wina aliyense koma tinangopeza akavalo okha pamodzi ndi abulu ali chimangire.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nadza iwo, naitana mlonda wa mudzi, namfotokozera; ndi kuti, Tinafika ku misasa ya Aaramu, ndipo taonani, palibe munthu pomwepo, kapena mau a munthu, koma akavalo omanga, ndi aburu omanga, ndi mahema ali cimangire.