2 Kings 7:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo mfumu idadzuka usiku nikauza nduna zake kuti, “Ndikuuzeni zimene Asiriya atikonzera. Iwowo akudziŵa kuti ife tili ndi njala. Nchifukwa chake atuluka m'zithando kuti akabisale ku thengo. Choncho tikangotuluka mumzinda muno, iwowo atigwira amoyo ndipo aloŵa mumzinda muno.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Niuka mfumu usiku, ninena ndi anyamata ake, Ndikufotokozereni m'mene Aaramu atichitira ife. Adziwa kuti tagwidwa ndi njala, natuluka m'misasa, nabisala kuthengo, ndi kuti, Pamene atuluka m'mudzi tidzawagwira ndi moyo ndi kulowa m'mudzimo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu inadzuka usiku ndipo inawuza atsogoleri ake a ankhondo kuti, “Ndikukuwuzani zimene Aaramu atichitira ife. Akudziwa kuti tikufa ndi njala; kotero achoka mu msasa wawo kukabisala kuthengo ndi kuti, ‘Iwowa atuluka ndithu, ndipo ife tidzawagwira amoyo ndi kulowa mu mzindamo.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Niuka mfumu usiku, ninena ndi anyamata ace, Ndikufotokozereni m'mene Aaramu aticitira ife. Adziwa kuti tagwidwa ndi njala, laturuka m'misasa, nabisala kuurengo, ndi kuti, Pamene aturuka m'mudzi tidzawagwira ndi moyo ndi kulowa m'mudzimo.