2 Kings 7:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma mmodzi mwa nduna zake adati, “Anthu a mumzinda muno posachedwa adzatsirizikanso monga Aisraele onse amene afa kaleŵa. Ndiye ife tiyeni tisankhe ena kuti atenge akavalo asanu amene atsalawo, tiŵatume kuti akaone.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nayankha mmodzi wa anyamata ake, nati, Atenge tsono akavalo otsala asanu, ndiwo otsala m'mudzi; taonani, adzanga unyinji wonse wa Israele otsalawo, kapena adzanga unyinji wonse wa Israele otsirizika; tiwatumize tione.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mmodzi mwa atsogoleri ake ankhondo anayankha kuti, “Chonde uzani anthu ena atenge akavalo asanu amene atsala mu mzinda muno. Taonani, zomwe zingawachitikire zidzakhala zofanana ndi zomwe zingachitikire ena onse amene atsala. Inde iwo adzangokhala ngati Aisraeli ena onse amene awonongeka kale. Choncho tiyeni tiwatume akafufuze zomwe zachitika.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nayankha mmodzi wa anyamata ace, nati, Atenge tsono akavalo otsala asanu, ndiwo otsala m'mudzi; taonani, adzanga unyinji wonse wa Israyeli otsalawo, kapena adzanga unyinji wonse wa Israyeli otsirizika; tiwatumize tione.