2 Kings 7:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero adasankha anthu aŵiri okwera pa akavalo, ndipo mfumuyo idaŵatuma kuti akalondole gulu la ankhondo la Asiriya. Idati, “Pitani mukaone chimene chachitika.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Motero anatenga magaleta awiri ndi akavalo ao; ndipo mfumu inawatumiza alondole khamu la Aaramu, ndi kuti, Mukani mukaone.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho anasankha magaleta awiri pamodzi ndi akavalo ake, ndipo mfumu inawatuma kuti alondole gulu lankhondo la Aaramu. Mfumuyo inalamula oyendetsa akavalowo kuti, “Pitani kaoneni.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Motero anatenga magareta awiri ndi akavalo ao; ndipo mfumu inawatumiza alondole khamu la Aaramu, ndi kuti, Mukani mukaone.