2 Kings 7:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu aja adaŵalondola Asiriya mpaka ku Yordani. Ndipo ndithu m'njira monse ankapeza zovala zili mbwee ndiponso katundu amene Asiriya ankapita nataya chifukwa cha kuthaŵa mofulumira. Pomwepo amithengawo adabwerera, nakauza mfumu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anawalondola mpaka ku Yordani; ndipo taonani, m'njira monse munadzala ndi zovala ndi akatundu adazitaya Aaramu m'kufulumira kwao. Nibwera mithenga, nifotokozera mfumu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthuwa anawalondola mpaka ku Yorodani, ndipo taonani, mʼnjira monse munali zovala zokhazokha ndi zinthu zimene Aaramu ankazitaya pamene ankathawa mofulumira. Ndipo amithengawo anabwerera ndi kudzafotokozera mfumu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anawalondola mpaka ku Yordano; ndipo taonani, m'njira monse munadzala ndi zobvala ndi akatundu adazitaya Aaramu m'kufulumira kwao. Nibwera mithenga, nifotokozera mfumu.