2 Kings 7:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono anthu a mu Samariya adatuluka nakafunkha ku zithando za Asiriya. Motero makilogramu atatu a ufa wosalala ankaŵagulitsadi pamtengo wa ndalama imodzi yasiliva, ndipo makilogramu asanu ndi limodzi a barele ankaŵagulitsanso chimodzimodzi potsata m'mene adaanenera Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Natuluka anthu, nafunkha m'misasa ya Aaramu. Ndipo anagula miyeso ya ufa ndi sekeli, nagulanso miyeso iwiri ya barele ndi sekeli, monga umo adanenera Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono anthu a mu Samariya anatuluka nakafunkha ku msasa wa Aaramu. Kotero kuti makilogalamu atatu a ufa ankawagulitsa pa mtengo wa ndalama imodzi yasiliva, ndipo makilogalamu asanu ndi limodzi a barele ankawagulitsanso pa mtengo wa ndalama imodzi yasiliva, monga momwe ananenera Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Naturuka anthu, nafunkha m'misasa ya Aaramu. Ndipo anagula miyeso wa ufa ndi sekeli, nagulanso miyeso iwiri ya barele ndi sekeli, monga umo adanenera Yehova.