2 Kings 7:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene zinkachitika zimenezi, nkuti mfumu itaika phungu wake wokhulupirika uja kuti akhale wolamulira pa chipata. Koma anthu adapondereza phunguyo kuchipata kuja, kotero kuti adafa, monga momwe Elisa munthu wa Mulungu adaanenera pamene mfumu idaapita kukamuwona.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma mfumu idayang'anitsa pachipata kazembe amene uja idafotsamira pa dzanja lake; ndipo anthu anampondereza pachipata, nafa iye, monga umo adanenera munthu wa Mulungu, ponena paja anamtsikira mfumu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono mfumu inayika mtsogoleri amene ankamudalira uja kuti akhale woyangʼanira pa chipata ndipo anthu anamupondaponda ku chipata kuja, ndipo anafa, monga momwe Elisa munthu wa Mulungu ananenera mfumu itapita ku nyumba yake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma mfumu idayang'anitsa pacipata kazembe amene uja idafotsamira pa dzanja lace; ndipo anthu anampondereza pacipata, nafa iye, monga umo adanenera munthu wa Mulungu, ponena paja anamtsikira mfumu.