2 Kings 7:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Paja mneneri Elisa adaauza mfumu kuti, “Makilogramu asanu ndi limodzi a barele adzaŵagulitsa pamtengo wa ndalama imodzi yasiliva, ndipo makilogramu atatu a ufa wosalala adzaŵagulitsanso pamtengo wa ndalama imodzi yasiliva maŵa pa nthaŵi ngati yomwe ino ku chipata cha Samariya.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunachitika, monga adanena munthu wa Mulungu kwa mfumu, ndi kuti, Adzagula miyeso iwiri ya barele ndi sekeli, adzagulanso muyeso wa ufa ndi sekeli; kudzatero mawa, dzuwa lino, pa chipata cha Samariya;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zinachitika molingana ndi zomwe ananena munthu wa Mulungu zija kuti “Mawa nthawi ngati yomwe ino, makilogalamu atatu a ufa adzawagulitsa pa mtengo wa ndalama imodzi yasiliva ndipo makilogalamu asanu ndi limodzi a barele adzawagulitsa pa mtengo wa ndalama imodzi yasiliva ku chipata cha Samariya.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunacitika, monga adanena munthu wa Mulungu kwa mfumu, ndi kuti, Adzagula miyeso iwiri ya barele ndi sekeli, adzagulanso muyeso wa ufa ndi sekeli; kudzatero mawa, dzuwa lino, pa cipata ca Samariya;