2 Kings 7:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo phungu wokhulupirika uja adaayankha Elisa munthu wa Mulungu uja, kuti, “Ngakhale Chauta mwiniwake atachita kutikhuthulira mvula yochuluka chotani, zoterezi nkuchitika ngati?” Apo mpamene Elisa adaamuuza kuti, “Ndithu udzaziwona zimenezo ndi maso ako, koma iweyo sudzazilaŵa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo kazembe uja adayankha munthu wa Mulunguyo, nati, Taonani tsono, Yehova angachite mazenera m'mwamba, chikachitika ichi kodi? Nati iye, Taona, udzachiona ichi ndi maso ako, koma osadyako ai;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mtsogoleriyu ananena kwa munthu wa Mulungu kuti, “Taona, ngakhale Yehova atatsekula zipata zakumwamba, kodi zimenezi zingachitikedi?” Munthu wa Mulungu anamuyankha kuti, “Iwe udzaziona zimenezi ndi maso ako, koma sudzadyako kanthu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo kazembe uja adayankha munthu wa Mulunguyo, nati, Taonani tsono, Yehova angacite mazenera m'mwamba, cikacitika ici kodi? Nati iye, Taona, udzaciona ici ndi maso ako, koma osadyako ai;